1 Tsegula pa makomo ako Lebano, kuti moto uthe mikungudza yako.
2 Cema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; cemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yocinjirizika yagwa pansi.
3 Mau a kucema kwa abusa! pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! pakuti kudzikuza kwa Yordano kwaipsidwa.
4 Atero Yehova Mulungu wanga: Dyetsani zoweta zakukaphedwa;
5 zimene eni ace azipha, nadziyesera osaparamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazicitira cifundo.
6 Pakuti sindidzacitiranso cifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wace, ndi m'dzanja la mfumu yace; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.