3 Ndipo Turo adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati pfumbi, ndi golidi woyenga ngati thope la kubwalo.
4 Taonani, Yehova adzamlanda zace, nadzakantha mphamvu yace igwe m'manja; ndipo adzatha ndi moto.
5 Asikeloni adzaciona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekroni, pakuti ciyembekezo cace cacitidwa manyazi; ndipo mfumu idzatayika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.
6 Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala m'Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti.
7 Ndipo ndidzacotsa mwazi wace m'kamwa mwace, ndi zonyansa zace pakati pa mano ace; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkuru wa pfuko m'Yuda, ndi Ekroni ngati Myebusi.
8 Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.
9 Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini cipulumutso; wofatsa ndi wokwera pa buru, ndi mwana wamphongo wa buru.