19 Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silvano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa iye.
20 Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa iye eya; cifukwa cacenso ali mwa iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.
21 Koma iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Kristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;
22 amenenso anatisindikiza cizindikilo, natipatsa cikole ca Mzimu mu mitima yathu.
23 Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kud kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.
24 Si kuti ticita ufumu pa cikhulupiriro canu, koma tikhala othandizana naco cimwemwe canu; pakuti ndi cikhulupiriro muimadi.