25 Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka combo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;
26 paulendo kawiri kawiri, moopsya mwace mwa mitsinje, moopsya mwace mwa olanda, 1 moopsya modzera kwa mtundu wanga, moopsya modzera kwa amitundu, moopsya m'mudzi, moopsya m'cipululu, moopsya m'nyanja, moopsya mwaabale onyenga;
27 m'cibvutitso ndi m'colemetsa, m'madikiro kawiri kawiri, 2 m'njala ndi ludzu, m'masalo a cakudyakawiri kawiri, m'cisanu ndi umarisece.
28 Popanda zakunjazo pali condisindikiza tsiku ndi tsiku, calabadiro ca Mipingo yonse.
29 3 Afoka ndani wosafoka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?
30 Ngati ndiyenerakudzitamandira, 4 ndidzadzitamandira ndi za kufoka kwanga.
31 Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, iye amene alemekezeka ku nthawi yonse, adziwa kuti sindinama.