4 mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unacititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti ciwalitsiro ca Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali cithunzithunzi ca Mulungu, cisawawalire.
5 Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Kristu Yesu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, cifukwa ca Kristu.
6 Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kuturuka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa ciwalitsiro ca cidziwitso ca ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.
7 Koma tiri naco cuma ici m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosacokera kwa ife;
8 ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi;
9 olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;
10 nthawi zonse tirikusenzasenza m'thupi kufa kwace kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi mwathu.