1 Ndipo a ocita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire cisomo ca Mulungu kwacabe inu,
2 (pakuti anena,M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe,Ndipo m'tsiku la cipulumutso ndinakuthandiza;Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la cipulumutso);
3 osapatsa cokhumudwitsa konse m'cinthu ciri conse, kuti utumikiwo usanenezedwe;
4 koma m'zonse tidzitsimikfzira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,
5 m'mikwingwirima, m'ndende, m'mapokoso, m'mabvutitso, m'madikiro, m'masalo a cakudya;
6 m'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'cikondi cosanyenga;