1 Ndipo tikudziwitsani, abale, cisomo ca Mulungu copatsika mwa Mipingo ya ku Makedoniya,
2 kuti m'citsimikizo cacikuru ca cisautso, kucurukitsa kwa cimwemwe cao, ndi kusauka kwaokweni kweni zidacurukira ku colemera ca kuolowa mtima kwao.
3 Pakuti monga mwa mphamvu yao, ndicitapo umboni, inde koposa mphamvu yao,
4 anacita eni ace, natiumirfza ndi kutidandauliraza cisomoco, ndi za ciyanjano ca utumiki wa kwa oyera mtima;