1 Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;
2 pakuti ndidziwa cibvomerezo canu cimene ndidzitamandira naco cifukwa ca inu ndi Amakedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu citapita caka; ndi cangu canu cinautsa ocurukawo.
3 Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pace m'menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;
4 kuti kapena akandiperekeze a ku Makedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingacititsidwe manyazi m'kulimbika kumene.
5 Cifukwa cace ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti cikhale cokonzeka comweci, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.