11 Ndi mfumu ya kumwela adzawawidwa mtima, nadzaturuka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukuru; koma unyinjiwo udzaperekedwa m'dzanja lace.
12 Ndipo ataucotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wace; ndipo adzagwetsa zikwi makumi makumi, koma sadzalakika.
13 Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wa kuposa oyamba aja; nidzafika pa cimariziro ca nthawi, ca zaka, ndi khamu lalikuru la nkhondo ndi cuma cambiri.
14 Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwela, ndi aciwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo.
15 Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda midzi yamalinga; ndi ankhondo a kumwela sadzalimbika, ngakhale anthu ace osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika.
16 Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzacita cifuniro cace ca iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pace; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwace mudzakhala cionongeko.
17 Ndipo adzalimbitsa nkhope yace, kudza ndi mphamvu ya ufumu wace wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzacita cifuniro cace, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kubvomerezana naye.