3 Ndipo idzauka mfumu yamphamvu, nidzacita ufumu ndi ulamuliro waukuru, nidzacita monga mwa cifuniro cace.
4 Ndipo pakuuka iye ufumu wace udzatyoledwa, nudzagawikira ku mphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yace akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wace anacita ufumu nao; pakuti ufumu wace udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.
5 Ndipo mfumu ya kumwela, ndiye wina wa akalonga ace, idzamposa mphamvu, nidzakhala nao ulamuliro; ulamuliro wace ndi ulamuliro waukuru.
6 Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwela adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lace; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lace; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija.
7 Koma apo pophukira mizu yace adzauka wina m'malo mwace, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzacita molimbana nao, nadzawalaka;
8 ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika za siliva ndi golidi adzazitenga kumka nazo ndende ku Aigupto; ndi zaka zace zidzaposa za mfumu ya kumpoto.
9 Ndipo adzalowa m'ufumu wa mfumu ya kumwela, koma adzabwera m'dziko lace lace.