3 Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate cilungamo ngati nyenyezi ku nthawi za nthawi.
4 Koma iwe Danieli, tsekera mau awa, nukomere cizindikilo buku, mpaka nthawi ya cimariziro; ambiri adzathamanga cauko ndi cauko, ndi cidziwitso cidzacuruka.
5 Pamenepo ine Danieli ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m'mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzace m'mphepete mwa mtsinje tsidya lija.
6 Ndipo wina anati kwa munthu wobvala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Cimariziro ca zodabwiza izi cidzafika liti?
7 Ndipo ndinamva munthuyo wobvala bafuta wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, nakweza dzanja lace lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzacitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.
8 Ndinacimva ici, koma osacizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, citsiriziro ca izi nciani?
9 Ndipo anati, Pita Danieli; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa cizindikilo mpaka nthawi ya citsiriziro.