10 Cifukwa ca mau a mfumu ndi akuru ace mkazi wamkuru wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakubvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;
11 pali munthu m'ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkuru wa alembi, openda, Akasidi, ndi alauli;
12 popeza m'Danieli yemweyo, amene mfumu adamucha Belitsazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi cidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa, ndi kumasula mfundo. Amuitane Danieli tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.
13 Pamenepo analowa naye Danieli kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Danieli, Ndiwe kodi Danieli uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?
14 Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana.
15 Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace; koma sanakhoza kufotokozera kumasulira kwa cinthuci.
16 Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace, udzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwo.