13 Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Danieli uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena coletsa munacitsimikizaco; koma apempha pemphero lace katatu tsiku limodzi.
14 Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wace pa Danieli kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.
15 Koma anthu awa anasonkhana kwa mfumu, nati kwa mfumu, Dziwani, mfumu, kuti lamulo la Amedi ndi Aperisi, ndilo kuti coletsa ciri conse ndi lemba liri lonse idazikhazikira mfumu, zisasinthike.
16 Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Danieli, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Danieli, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.
17 Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi cosindikizira cace, ndi cosindikizira ca akuru ace, kuti kasasinthike kanthu ka Danieli.
18 Pamenepo mfumu inamuka ku cinyumba cace, nicezera kusala usikuwo, ngakhale zoyimbitsa sanabwera nazo pamaso pace, ndi m'maso mwace munamuumira.
19 Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira ku dzenje la mikango.