1 MAU a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, caka ca makumi awiri, pokhala ine ku Susani ku nyumba ya mfumu,
2 anafika Hanani, mmodzi wa abale anga, iye ndi amuna ena a ku Yuda; ndipo ndinawafunsa za Ayuda adapulumukawo otsala andende, ndi za Yerusalemu.
3 Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko ku dzikoko akulukutika kwakukuru, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zace zatenthedwa ndi moto.
4 Ndipo kunali, pakumva'mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kucita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,
5 ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace;