1 MAU a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, caka ca makumi awiri, pokhala ine ku Susani ku nyumba ya mfumu,
2 anafika Hanani, mmodzi wa abale anga, iye ndi amuna ena a ku Yuda; ndipo ndinawafunsa za Ayuda adapulumukawo otsala andende, ndi za Yerusalemu.
3 Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko ku dzikoko akulukutika kwakukuru, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zace zatenthedwa ndi moto.
4 Ndipo kunali, pakumva'mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kucita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,
5 ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace;
6 muchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israyeli akapolo anu, ndi kuulula zoipa za ana a Israyeli zimene tacimwira nazo Inu; inde tacimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.
7 Tacita mwamphulupulu pa Inu, osasunga malamulo, kapena malemba, kapena maweruzo, amene mudalamulita mtumiki wanu Mose.