5 ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace;
6 muchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israyeli akapolo anu, ndi kuulula zoipa za ana a Israyeli zimene tacimwira nazo Inu; inde tacimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.
7 Tacita mwamphulupulu pa Inu, osasunga malamulo, kapena malemba, kapena maweruzo, amene mudalamulita mtumiki wanu Mose.
8 Mukumbukile mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu;
9 koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwacita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kucokera komweko, ndi kubwera nao ku malo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.
10 Ndipo awa ndi akapolo anu ndi anthu anu, amene munawaombola ndi mphamvu yanu yaikuru, ndi dzanja lanu lolimba.
11 Yehova, mucherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mulemereze kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera cifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu cakumwa cace.