Nehemiya 10:32-38 BL92

32 Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka caka ndi caka limodzi la magawo atatu a sekeli ku nchito ya nyumba ya Mulungu wathu;

33 kuliperekera mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israyeli zoipa, ndi nchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.

34 Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a copereka ca nkhuni, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika caka ndi caka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'cilamulo;

35 ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uli wonse caka ndi caka, ku nyumba ya Yehova;

36 ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'cilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;

37 ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uli wonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, ku zipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzi limodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.

38 Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzi limodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzi limodzi la magawo khumi ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, ku nyumba ya cuma.