36 ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'cilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;
37 ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uli wonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, ku zipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzi limodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.
38 Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzi limodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzi limodzi la magawo khumi ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, ku nyumba ya cuma.
39 Pakuti ana a Israyeli ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oyimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.