18 wa Biliga, Samura; wa Semaya, Yehonatani;
19 ndi wa Yoyaribi, Matani; wa Yedaya, Uzi;
20 wa Salai, Kalai; wa Amoki, Eberi;
21 wa Hilikiya, Hasabiya; wa Yedaya, Netaneli.
22 M'masiku a Ehasibi, Yoyada, Yohanana, ndi Yoduwa, Alevi analembedwa akuru a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariyo wa ku Perisiya.
23 Ana a Levi, akuru a nyumba za makolo, analembedwa m'buku la macitidwe, mpaka masiku a Yohanana mwana wa Eliasibu.
24 Ndi akuru a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.