28 Ana a oyimbirawo anasonkhana ocokera ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku midzi ya Anetofati,
29 ndi ku Betegiligala, ndi ku minda ya Geba ndi Azimaveti; popeza oyimbirawo adadzimangira midzi pozungulira Yerusalemu.
30 Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga.
31 Pamenepo ndinakwera nao akuru a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akuru oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kumka ku cipata ca kudzala;
32 ndi pambuyo pao anayenda Hosaya, ndi limodzi la magawo awiri a akuru a Yuda,
33 ndi Azariya, Ezara ndi Mesulamu,
34 Yuda, ndi Benjamini, ndi Semaya, ndi Yeremiya,