7 ndipo ndinafika ku Yerusalemu, ndi kuzindikira coipa anacicita Eliasibu, cifukwa ca Tobiya, ndi kumkonzera cipinda m'mabwalo a nyumba ya Mulungu.
8 Ndipo ndinaipidwa naco kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwacotsa m'cipindamo.
9 Pamenepo ndinalamulira, ndipo anayeretsa zipindazo; ndipo ndinabwezeramonso zipangizo za nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za ufa ndi libano.
10 Ndinazindikiranso kuti sanapereka kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oyimbira adathawira yense ku munda wace.
11 Potero ndinatsutsana nao olamulira, ndinati, Yasiyidwiranji nyumba ya Mulungu? Ndipo ndinawasonkhanitsa, ndi kuwafka m'malo mwao.
12 Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzi limodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ku nyumba za cuma.
13 Ndinaikanso osunga cuma, asunge nyumba za cuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao.