1 Koma kunacitika mwezi wa Nisana, caka ca makumi awiri ca Aritasasta mfumu pokhala vinyo pamaso pace, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wacisoni pamaso pace ndi kale lonse.
2 Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja cisoni cifukwa ninji popeza sudwala? ici si cinthu cina koma cisoni ca mtima. Pamenepo ndinacita mantha akuru.
3 Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kucita cisoni, popeza pali bwinja kumudzi kuli manda a makolo anga, ndi zipata zace zopsereza ndi moto.
4 Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.