10 Atamva Sanibalati Mhoroni, ndi Tobiya kapoloyo M-amoni, cidawaipira kwakukuru, kuti wadza munthu kuwafunica ana a Israyeli cokoma.
11 Motero ndinafika ku Yerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu.
12 Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine coika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndicitire Yerusalemu; panalibenso nyama yina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.
13 Ndipo ndinaturuka usiku pa cipata ca kucigwa, kumka ku citsime ca cinjoka, ndi ku cipata ca kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zace zothedwa ndi moto.
14 Ndipo ndinapitima kumka ku cipata cacitsime, ndi ku dziwe la mfumu; koma popita nyama iri pansi panga panaicepera.
15 Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa cipata ca kucigwa, momwemo ndinabwereranso.
16 Koma olamulira sanadziwa uko ndinamuka, kapena cocita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufuru, kapena olamulira, kapena otsala akucita nchitoyi.