8 napangana ciwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kucita cisokonezo m'menemo.
9 Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, cifukwa ca iwowa.
10 Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi licuruka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.
11 Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa nchitoyi.
12 Ndipo kunali, atafika Ayuda okhala pafupi pao ocokera pamalo ponse, anatiuza ife kakhumi, Bwererani kwa ife.
13 Cifukwa cace ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.
14 Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukilani Yehova wamkuru ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu amuna ndi akazi, akazi anu, ndi nyumba zanu.