3 Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndirikucita nchito yaikuru, sindikhoza kutsika; ndiidulirenji padera nchito poileka ine, ndi kukutsikirani?
4 Nanditumizira ine mau otere kanai; ndinawabwezeranso mau momwemo.
5 Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wace kwa ine kacisanu, ndi kalata wosatseka m'dzanja mwace;
6 m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gasimu acinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; cifukwa cace mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.
7 Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.
8 Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako.
9 Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka nchito, ndipo siidzacitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.