8 Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako.
9 Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka nchito, ndipo siidzacitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.
10 Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane ku nyumba ya Mulungu m'kati mwa Kacisi, titsekenso pa makomo a Kacisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe.
11 Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? ndani wonga ine adzalowa m'Kacisi kupulumutsa moyo wace? sindidzalowamo.
12 Ndipo ndinazindikira kuti sanamtuma Mulungu; koma ananena coneneraco pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera.
13 Anamlembera cifukwa ca ici, kuti ine ndicite mantha, ndi kucita cotero, ndi kucimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.
14 Mukumbukile, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa nchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.