5 Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyeli, Buni, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petatiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu ku nthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa cilemekezo ndi ciyamiko conse.
6 Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse ziri pomwepo, nyanja ndi zonse ziri m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu la kumwamba lilambira Inu.
7 Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumturutsa m'Uri wa Akasidi, ndi kumucha dzina lace Abrahamu;
8 ndipo munampeza mtima wace wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zace; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.
9 Ndipo munapenya msauko wa makolo athu m'Aigupto, nimunamva kupfuula kwao ku Nyanja Yofiira,
10 nimunacitira zizindikilo ndi zodabwiza Farao ndi akapolo ace onse, ndi anthu onse a m'dziko lace; popeza munadziwa kuti anawacitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.
11 Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.