9 Ndipo munapenya msauko wa makolo athu m'Aigupto, nimunamva kupfuula kwao ku Nyanja Yofiira,
10 nimunacitira zizindikilo ndi zodabwiza Farao ndi akapolo ace onse, ndi anthu onse a m'dziko lace; popeza munadziwa kuti anawacitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.
11 Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.
12 Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.
13 Munatsikiranso pa phiri la Sinai, nimunalankhula nao mocokera m'Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi cilamulo coona, malemba, ndi malamulo okoma;
14 ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi cilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
15 ndi mkate wocokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi oturuka m'thanthwe munawaturutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.