11 Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamcisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala cete, lipumula.
12 Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osacitira cifundo Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?
13 Ndipo Yehova anamyankha mthenga wakulankhula ndi ine mau okoma, mau akutonthoza mtima.
14 Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Pfuula, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndicitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni ndi nsanje yaikuru.
15 Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukuru; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira coipa,
16 Cifukwa cace atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zacifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi cingwe.
17 Pfuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Midzi yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.