7 Tsiku la makumi awiri ndi cinai la mwezi wakhumi ndi cimodzi, ndiwo mwezi wa Segati, caka caciwiri ca Dariyo, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,
8 Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamcisu inali kunsi; ndi pambuyo pace panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.
9 Pamenepo ndinati, Awa ndi ciani, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi ciani.
10 Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamcisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m'dziko.
11 Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamcisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala cete, lipumula.
12 Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osacitira cifundo Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?
13 Ndipo Yehova anamyankha mthenga wakulankhula ndi ine mau okoma, mau akutonthoza mtima.