12 Koma ici ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Kristu.
13 Kodi Kristu wagawika? Kodi Paulo anapacikidwa cifukwa ca inu? Kapena kodi munabatizidwa m'dzina la Paulo?
14 Ndiyamika Mulungu kuti sindinabatiza mmodzi yense wa inu, koma Krisipo ndi Gayo;
15 kuti anganene mmodzi kuti mwabatizidwa m'dzina langa.
16 Koma ndinabatizanso a pa banja la Stefana; za ena, sindidziwa ngati ndinabatiza wina yense.
17 Pakuti Kristu sanandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Kristu ungayesedwe wopanda pace.
18 Pakuti mau a mtanda ali ndithu cinthu copusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tirikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.