1 Akorinto 10 BL92

Tisayese dala Mulungu monga Israyeli

1 Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;

2 nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja,

3 nadya onse cakudya cauzimu cimodzimodzi;

4 namwa onse cakumwa cauzimu cimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Kristu.

5 Koma ocuruka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'cipululu.

6 Koma zinthu izi zinacitika, zikhale zoticenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.

7 Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.

8 Kapena tisacite dama monga ena a iwo anacita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.

9 Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.

10 Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo.

11 Koma izi zinacitika kwa iwowa monga zoticenjeza, ndipo zinalembedwa kuticenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.

12 Cifukwa cace iyewakuyesa kuti ali ciriri, ayang'anire kuti angagwe,

13 Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Za kupembedza mafano, za kuyanjana ndi ziwanda

14 Cifukwa cace, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

15 Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu cimene ndinena.

16 Cikho ca dalitso cimene tidalitsa, siciri ciyanjano ca mwazi wa Kristu kodi? Mkate umene tinyema suli ciyanjano ca thupi la Kristu kodi?

17 Pakuti mkate ndiwo umodzi, cotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako ku mkate umodzi.

18 Tapenyani Israyeli monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe ciyanjano ndi guwa la nsembe?

19 Ndinena ciani tsono? kuti coperekedwa nsembe kwa mafano ciri kanthu? Kapena kuti fane liri kanthu kodi?

20 Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

21 Simungathe kumwera cikho ca Ambuye, ndi cikho ca ziwanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda.

22 Kapena kodi ticititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa iye?

Mkristu ndiye mfulu koma wosamalira ena

23 Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

24 Munthu asafune zace za iye yekha, kama za mnzace.

25 Conse cogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu cifukwa ca cikumbu mtima;

26 pakuti dziko lapansi liri la Ambuye, ndi kudzala kwace.

27 Ngati wina wa osakhulupira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye comwe ciikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, cifukwa ca cikumbu mtima.

28 Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, cifukwa ca iyeyo wakuuza, ndi cifukwa ca cikumbu mtima.

29 Ndinena cikumbu mtima, si ca iwe mwini, koma ca winayo; 1 pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi cikumbu mtima ca wina?

30 Ngati ine ndilandirako mwacisomo, ndinenezedwa bwanji cifukwa ca ici cimene ndiyamikapo?

31 Cifukwa cace 2 mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

32 3 Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Ahelene, kapena Mpingo wa Mulungu;

33 monga 4 inenso ndikodweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna cipindulo canga, koma ca unyinjiwo, kuti apulumutsidwe.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16