1 Kwamveka ndithu kuti kuli cigololo pakati pa inu, ndipo cigololo cotere conga sicimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wace.
2 Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwacita cisoni, kuti acotsedwe pakati pa inu iye amene anacita nchito iyi.
3 Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndiripo,
4 m'dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,
5 kumpereka iye wocita cotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.
6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti cotupitsa pang'ono citupitsa mtanda wonse?
7 Tsukani cotupitsa cakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paskha wathu waphedwa, ndiye Kristu;
8 cifukwa cace ticita phwando, si ndi cotupitsa cakale, kapena ndi cotupttsaca dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi coonadi.
9 Ndinalembera inu m'kalata uja, kuti musayanjane ndi acigololo;
10 si konse konse ndi acigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukaturuke m'dziko lapansi;
11 koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wochedwa mbale ali wacigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.
12 Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m'katimosimuwaweruza ndi inu,
13 komaakunia awaweruza Mulungu? Cotsani woipayo pakati pa inu nokha.