1 Akorinto 9 BL92

Ululu ndi ulamuliro wa mtumwiyo

1 Kodi sindine mfulu? Kodi slndine mtumwi? Kodi sindinaona Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu nchito yanga mwa Ambuye?

2 Ngati sindiri mtumwi kwa ena, komatu ndiri kwa inu; pakuti cizindikilo ca utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.

3 Codzikanira canga kwa iwoamene andifunsa ine ndi ici:

4 Kodi tiribe ulamuliro wa kudya ndi kumwa?

5 Kodi tiribe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?

6 Kapena kodi ife tokha, Bamaba ndi ine, tiribe ulamuliro wakusagwira nchito?

7 Msilikari ndani acita nkhondo, nthawi iriyonse, nadzifunira zace yekha? Aoka mipesa ndani, osadya cipatso cace? Kapena aweta gulu ndani, osadyamkaka wace wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?

8 Kapena cilamulo sieinenanso zomwezo?

9 Pakuti m'cilamulo ca Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe?

10 Kapena acinena ici konse konse cifukwa ca ife? Pakuti, cifukwa ca ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa ciyembekezo, ndi wopunthayo acita mwa ciyembekezo ca kugawana nao.

11 Ngati takufeserani inu zauzimu, kodi ncacikuru ngati ife tituta za thupi lanu?

12 Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinacita nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingacite cocedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Kristu,

13 Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za kacisi amadya za m'Kacisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

14 Comweconso Ambuyeanalamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

Kudzipereka kwa mtumwiyo; Makani a liwiro a Mkristu

15 Koma ine sindinacita nako kanthu kaizi; ndipo sindilemba izi kuti cikakhale cotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwacabe kudzitamanda kwanga.

16 Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndiribe kanthu kakudzitamandira; pakuti condikakamiza ndigwidwa naco; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira U thenga Wabwino.

17 Pakuti ngati ndicita ici cibvomerere, mphotho ndiri nayo; koma ngati si cibvomerere; anandikhulupirira m'udindo.

18 Mphotho yanga nciani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.

19 Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ocuruka.

20 Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;

21 kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo twa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.

22 Kwa ofoka ndinakhala ngati wofoka, kuti ndipindule ofoka, Ndakhala zonse kwa anthu onse, 1 kuti pali ponse ndikapulumutse ena.

23 Koma ndicita zonse zifukwa ca Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

24 Kodi umudztwa kuti iwo akucita makani a Iwiro, athamangadi onse, koma nmodzi alandira mfupo? Motero 2 thamangani, kuti mukalandire.

25 Koma yense wakuyesetsana adzikaniza zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakubvunda; 3 koma ife wosabvunda.

26 Cifukwa cace ine ndithamanga cotero, si nonga cosinkhasinkha. Ndilimbaaa cotero, si monga ngati kupanda nlengalenga;

27 koma 4 ndipumpuatha thupi langa, ndipo ndiliyesa capolo; kuti, kapena ngakhale rdalalikira kwa ena, 5 ndingakhale votayika ndekha.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16