1 Akorinto 1 BL92

1 PAULO, woitanidwa akhale mtumwi wa Yesu Kristu mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Sositene mbaleyo,

2 kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m'Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Kristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:

3 Cisomo kwa inu ndi mtendere zocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.

4 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, cifukwa ca cisomo ca Mulungu cinapatsidwa kwa inu mwa Kristu Yesu;

5 kuti m'zonse muoalemezedwa mwa iye, m'mau onse, ndi cidziwitso conse;

6 mongaumboni wa Kristu unakhazikika mwa inu;

7 kotero kuti sicikusowani inu caufuru ciri conse; pakulindira inu bvumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu;

8 amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira cimariziro, kuti mukhale opanda cifukwa m'tsiku la Ambuye: wathu Yesu Kristu.

9 Mulungu ali, wokhulupirika amene munaitanidwa mwa iye, ku ciyanjano ca Mwana wace Yesu Kristu, Ambuye wathu.

Malekano mu Mpingo wa ku Korinto

10 Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene cimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'ciweruziro comweco.

11 Pakuti zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu.

12 Koma ici ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Kristu.

13 Kodi Kristu wagawika? Kodi Paulo anapacikidwa cifukwa ca inu? Kapena kodi munabatizidwa m'dzina la Paulo?

14 Ndiyamika Mulungu kuti sindinabatiza mmodzi yense wa inu, koma Krisipo ndi Gayo;

15 kuti anganene mmodzi kuti mwabatizidwa m'dzina langa.

16 Koma ndinabatizanso a pa banja la Stefana; za ena, sindidziwa ngati ndinabatiza wina yense.

Nzeru za Mulungu ndi nzeru za anthu

17 Pakuti Kristu sanandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Kristu ungayesedwe wopanda pace.

18 Pakuti mau a mtanda ali ndithu cinthu copusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tirikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.

19 Pakuti kulembedwa,Ndidzaononga nzeru za anzeru,Ndi kucenjerakwa ocenjera odidzakutha.

20 Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi?

21 Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yace, silinadziwa Mulungu, cidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirawo mwa copusa ca kulalikira.

22 Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikilo, ndi Ahelene atsata nzeru:

23 koma ife tilalikira Kristu wopacikidwa, kwa Ayudatu cokhumudwitsa, ndi kwa amitundu cinthu copusa;

24 koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Kristu 1 mphamvu ya Mulungu, ndi 2 nzeru ya Mulungu.

25 Cifukwa kuti copusa ca Mulungu ciposa anthu ndi nzeru zao; ndipo cofoka ca Mulunguciposa anthu ndi mphamvu yao.

26 Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti 3 saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai;

27 koma 4 Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akacititse manyazi anzeru; ndipo zofoka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akacititse manyazi zamphamvu;

28 ndipo zopanda pace za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; 5 kuti akathere zinthu zoti ziriko;

29 6 kuti thupi liri lonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.

30 Koma kwa iye muli inu mwa Kristu Yesu, 7 amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi cilungamo ndi ciyeretso ndi ciombolo;

31 kuti monga mwalembedwa, iye amene adzitamanda, adzitamande mwa Ambuye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16