1 Akorinto 7 BL92

Mau a za ukwati

1 Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.

2 Koma cifukwa ca madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

3 Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ace; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna.

4 Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lace la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi laiye yekha, koma mkazi ndiye.

5 Musakanizana, koma ndi kubvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, cifukwa ca kusadziletsa kwanu.

6 Koma ici ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira.

7 Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndiri ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yace ya iye yekha kwa Mulungu, wina cakuti, wina cakuti.

8 Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.

9 Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.

10 Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,

11 komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.

12 Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkaziwosakhulupira, ndipo iye abvomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.

13 Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupira, nabvomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo.

14 Pakuti mwamuna wosakhulupirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.

15 Koma ngati wosakhulupirayo acoka, acoke. M'mirandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo, Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.

16 Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?

17 Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika m'Mipingo yonse.

18 Kodi waitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe.

19 Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.

20 Yense akhale m'maitanidwe m'mene anaitanidwamo.

21 Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, cita nako ndiko.

22 Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Kristu.

23 Munagulidwa ndi mtengo wace; musakhale akapolo a anthu.

24 Yense, m'mene anaitanidwamo, abate, akhale momwemo ndi Mulungu.

25 Koma kunena za anamwali, ndiribe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani coyesa ine, monga wolandira cifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.

26 Cifukwa cace ndiyesa kuti ici ndi cokoma cifukwa ca cibvuto ca nyengo yino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali.

27 Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.

28 Koma ungakhale ukwatira, sunacimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanacimwa. Koma otere adzakhala naco cisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.

29 Koma ici nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;

30 ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;

31 ndi iwo akucita nalo dziko lapansi, monga ngati osacititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.

32 Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye;

33 koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wace.

34 Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso iye wosakwatiwa alabadira za. Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.

35 Koma ici ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakuchereni msampha, koma kukuthandizani kucita cimene ciyenera, ndi kutsata citsatire Ambuye, opanda coceukitsa.

36 Koma wina akayesa kuti acitira mwana wace wamkazi cosamuyeoera, ngati palikupitirira pa unamwali wace, ndipo kukafunika kutero, acite cimene afuna, sacimwa; akwatitsidwe.

37 Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwace, wopanda cikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa cifuniro ca iye yekha, natsimikiza ici mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wace wamkazi, adzacita bwino.

38 Cotero iye amene akwatitsa mwana wace wamkazi acita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa acita koposa.

39 Mkazi amangika pokhala mwamuna wace ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.

40 Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndiganiza kuti inenso ndiri naye Mzimu wa Mulungu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16