1 Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe cikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
2 Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri naco cikhulupiriro conse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe cikondi, ndiri cabe.
3 Ndipo ndingakhale ndipereka cuma cangaconsekudyetsa osauka, ndipo ndingakhalendipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndiribe cikondi, sindipindula kanthu ai.
4 Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza,
5 sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa;
6 sicikondwera ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;
7 cikwirira zinthu zonse, cfkhulupirira zinthu zonse, ciyembekeza zinthu zonse, cipirira zinthu zonse.
8 Cikondi sicitha nthawizonse, koma kapena zonenera zidzakhala cabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala cabe.
9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.
10 Koma pamene cangwiro cafika, tsono camderamdera cidzakhalacabe.
11 Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa cabe zacibwana.
12 Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati cimbuuzi; koma R pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.
13 Ndipo tsopano zitsala cikhulupiriro, dyembekezo, cikondi, zitatu izi; koma cacikuru ca izi ndico cikondi.