1 Akorinto 6 BL92

Awadzudzula pa mirandu ya pakati pa abale

1 Kodiakhoza winawa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzace, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?

2 Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tocepacepa?

3 Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? koposa kotani nanga zinthu za moyo uno?

4 Cifukwa cace, ngati muli nayo mirandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa acabe mu Mpingo?

5 Ndinena ici kukucititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,

6 koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupira?

7 Koma pamenepo pali cosowa konse konse mwa inu, kuti muli nayo mirandu wina ndi mnzace. Cifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? simusankhula cifukwa ninji kulolakunyengedwa?

8 Koma muipsa, nimunyenga, ndipo mutero nao abale anu.

9 Kapenasimudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasoceretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena acigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,

10 kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

11 Ndipo ena ainu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Matupi athu ali ziwalo za Kristu

12 Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula, Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa naco cimodzi.

13 Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi siliri la cigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;

14 koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yace.

15 Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Kristu? cifukwa cace ndidzatenga ziwalo za Kristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi waciwerewere? Msatero iai.

16 Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi waciwerewere ali thupi limodzi? Pakuti, awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.

17 Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi.

18 Thawani dama. Cimo liri lonse munthu akalicita liri kunja kwa thupi; koma waciwerewere acimwira thupi lace la iye yekha.

19 Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

20 Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16