1 Akorinto 14 BL92

Mpnatso ya kunenera tposa ya malilime

1 Tsatani cikondi; koma funitsitsani mphatsozauzimu, koma koposa kuti mukanenere.

2 Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibemunthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.

3 Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu comangirira ndi colimbikitsa, ndi cosangalatsa,

4 Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo.

5 Ndipo ndifuna inu nonse mula'nkhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire comangirira.

6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikaku, pindulitsani ciani, ngati sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso, kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitsot

7 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, cidzazindikirikabwanji cimene ciombedwa kapena kuyimbidwa?

8 Pakuti ngad Lipenga lipereka mao osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?

9 Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji cimene cilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.

10 Iripo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.

11 Cifukwa cace, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwaine.

12 Momwemo inunso, popeza muli ofunits its a mphatso zauzimu, funani kuti mukacuruke kukumangirira kwa Mpingo,

13 Cifukwa cace wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.

14 Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma cidziwitso canga cikhala cosabala kanthu.

15 Kuli ciani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi cidziwitso canga; ndidzayimba ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi cidziwitso.

16 Cifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa cimene unena?

17 Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwa.

18 Ndiyanillca Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;

19 koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.

20 Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda, koma m'cidziwitso akulu misinkhu.

21 Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

22 Cotero malilime akhala ngati cizindikilo, si kwa iwo akukhulupira, koma kwa iwo osakhulupira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupira, koma kwa two amene akhulupira.

23 Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka?

24 Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

25 zobisika za mtima wace zionetsedwa; ndipo cotero adzagwa nkhope yace pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.

Cipembedzo cicitike molongosoka

26 Nanga ciani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo, ali naco ciphunzitso, ali nalo bvumbulutso, ali nalo lilime, ali naco cimasuliro. Mucite zonse kukumangirira.

27 Ngati wina alankhula lilime, acite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.

28 Koma ngati palibe womasulira, akhale cete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.

29 Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire.

30 Koma ngati kanthu kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale cete woyambayo.

31 Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzi mmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;

32 ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;

33 pakuti Mulungu sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.

34 Akazi akhale cete m'Mipingo. Pakuti vsikuloledwa kwa iwo kulankhula, Koma akhale omvera, mongansocilamulo cmena,

35 Koma ngati afuna kuphunzirakanthu afunseamuna ao aiwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.

36 Kodi mau a Mulungu anatutuka kwa iw? kapena anafika kwa inu nokha?

37 Ngatiwinaayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu; azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye,

38 Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.

39 Cifukwa cace; abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.

40 Koma zonse zicitike koyenera ndi kolongosoka.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16