1 Akorinto 11 BL92

1 Khalani onditsanza ine, monga inenso oditsanza Kristu.

Za akazi m'Eklesia wa Ambuye

2 Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukila ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.

3 Koma ndifunakuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu,

4 Mwamuna yense wobveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wace.

5 Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wobvula mutu, anyoza mutu wace; pakuti kuli cimodzimodzi kumetedwa.

6 Pakuti ngati mkazi sapfunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kucititsa manyazi, apfunde,

7 Pakuti mwamuna sayenera kubvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

8 Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;

9 pakutinso mwamuna sanalengedwa cifukwa ca mkazi;

10 koma mkazi cifukwa ca mwamuna; cifukwa ca ici mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pace, cifukwa ca angelo.

11 Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.

12 Pakuti monga mkazi aliwa kwa mwamuna, comweconso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse ziri za kwa Mu, lungu.

13 Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosapfunda mutu?

14 Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi cimnyozetsa iye?

15 Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lace lapatsidwa kwa iye ngati cophimba.

16 Koma akaoneka wina ngati wotetana, tiribe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Eklesia wa Mulungu.

Zosayenera pa madyerero a cikondi. Macitidwe a Mgonero wa Ambuye

17 Koma pakulalikira ici sinditama inu, popeza simusonkhanira cokoma, koma coipa.

18 Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndibvomereza penapo.

19 Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo obvomerezedwa aonetsedwemwa inu.

20 Cifukwa cace, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;

21 pakuti pakudyaku yense athanga watenga mgonero wace wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.

22 Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Eklesia wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena ciani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.

23 Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, cimenenso ndinapereka kwainu, kuti Ambuye Yesu usikuuja anaperekedwa, anatenga mkate;

24 ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, ici ndi thupi langa la kwa inu; citani ici cikhale cikumbukilo canga.

25 Koteronso cikho, citatha cakudya, ndi kuti, Cikho ici ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; citani ici, nthawi zonse mukamwa, cikhale cikumbukilo canga,

26 Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera cikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.

27 Cifukwa cace yense amene akadyamkate, kapena akamwera cikho ca Ambuye kosayenera, adzakhala wocimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.

28 Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera cikho.

29 Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa ciweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.

30 Cifukwa cace ambiri mwa inu afoka, nadwala, ndipo ambiri agona.

31 Koma ngati tikadadzizindikira tokha sitikadaweruzidwa.

32 Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.

33 Cifukwa cace, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani.

34 Ngati wina ali ndi njala adye-kwao; kuti mungasonkhanire kwa ciweruziro. Koma zotsalazo nelidzafotokoza pakudza ine.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16