1 Akorinto 2 BL92

Ulalikidwe wa Paulo

1 Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu cinsinsi ca Mulungu.

2 Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu koma Yesu Kristu, ndi iye wopacikidwa.

3 Ndipo ine ndinakhala nanu mofoka ndi m'mantha, ndi monthunthumira mwambiri.

4 Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma m'cionetso ca Mzimu ndi ca mphamvu;

5 kuti cikhulupiriro canu cisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.

6 Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi yino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi yino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;

7 koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'cinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,

8 imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi a pansi pano; pakuti akadadziw sakadapaeika Mbuye wa ulemerero

9 koma monga kulembedwa,Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva,Nisizinalowa mu mtima wa munthu,Zimene ziri zonse Mulungi anakonzereratu iwo aku mkonda iye.

10 Koma kwa ife Mulungu anati onetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.

11 Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

12 Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.

13 Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.

14 Koma munthu wa cibadwidwe ca umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, cifukwa ziyesedwa mwauzimu.

15 Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense.

16 Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize iye? Koma ife tiri nao mtima wa Kristu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16