1 Akorinto 15 BL92

Za kuuka kwa akufa

1 Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo,

2 umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupira cabe.

3 Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, cimenenso ndinalandira, kuti Kristuanafera zoipa zathu, mongamwa malembo;

4 ndi kuti anaikidwa; ndi kutianaukitsidwa tsiku lacitatu, monga mwa malembo;

5 ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;

6 pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ocuruka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;

7 pomwepoanaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa: atumwi onse;

8 ndipo potsiriza pace pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.

9 Pakuti ine ndiri wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kuchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu.

10 Koma ndi cisomo ca Mulungu ndiri ine amene ndiri; ndipo cisomo cace ca kwa ine sicinakhala copanda pace, koma ndinagwirira nchito yocuruka ya iwo onse; koma si ine, komacisomo ca Mulungu cakukhala ndi ine.

11 Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupira.

12 Koma ngati Kristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanjikuti kulibe kuuka kwa akufa?

13 Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristunso sanaukitsidwa;

14 ndipo ngati Kristu sanaukitsidwakulalikira kwathu kuli cabe, cikhulupiriro canunso ciri cabe.

15 Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; cifukwa n tinacita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Kristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa,

16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Kristunso sanaukitsidwa;

17 ndipo ngati Kristu sanaukitsidwa, cikhulupiriro canu ciri copanda pace; muli cikhalire m'macimo anu.

18 Cifukwa cace iwonso akugona mwa Kristu anatayika.

19 Ngati tiyembekezera Kristu m'moyo uno wokha, tiri ife aumphawi oposa a anthu onse,

20 Koma tsopano Kristu waukitsidwa kwa akufa, cipatso coundukula ca iwo akugona.

21 Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.

22 Pakuti mongamwa Adamu onse amwalira, coteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.

23 Koma yense m'dongosolo lace la iye yekha, cipatso coundukula Kristu, pomwepo iwo a Kristu, pa kubwera kwace.

24 Pomwepo pali cimariziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera ciweruzo conse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.

25 Pakuti ayenera kucita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ace.

26 Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.

27 Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace. Koma pamene anena kutizonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.

28 Ndipo pamene zonsezo: zagonjetsedwa kwa iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa iye amene anamgonjetsera zinthuzonse; kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.

29 Ngati si kutero, adzacita ciani iwo amene abatizidwa cifukwa ca akufa? Ngatiakufa saukitsidwa konse, abatizidwa cifukwa ninji cifukwa ca iwo?

30 Nanga 1 ifenso tiri m'moopsya bwanji nthawi zonse?

31 2 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndiri nako mwa Kristu Yesu, Ambuye wathu.

32 3 Ngati odinalimbana ndi zirombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, 4 tidye timwepakuti mawa timwalira.

33 Musanyengedwe; 5 mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma

34 6 Ukani molungama, ndipo musacimwe; pakuti enaalibe cidziwitso ca Mulungu, Ndilankhula kunyaza inu.

35 Koma wina adzati, 7 Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalorhupi lotani?

36 Wopusa iwe, 8 cimene ucifesa wekha sieikhalitsi'dwanso camoyo, ngati sicifa;

37 ndipo cimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbeu yokhakapenaya tirigu kapena ya, mtundu wina;

38 koma Mulungu iaipatsa thupi mongaafuna; ndi, kwa mbeu yonse thupi lace lace.

39 Nyama yonse siiri imodzimodzi; koma yinandi Ya anthu, ndi yina ndiyo nyama ya zoweta, ndi yina ndiyo nyama ya mbalame, ndi yina ya nsomba.

40 Palinso matupi am'mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam'mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.

41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m'ulemerero.

42 9 Comweconso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'cibvundi, liukitsidwa m'cisabvundi;

43 10 lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa m'ulemerero; lifesedwa m'cifoko, liukitsidwa mumphamvu;

44 lifesedwa thupi Iacibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi Iacibadwidwe, palinso lauzimu.

45 Koteronso kwalembedwa, 11 Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. 12 Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.

46 Koma cauzimu siciri coyamba, koma cacibadwidwe; pamenepo cauzimu.

47 13 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu waciwiri ali wakumwamba.

48 14 Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba.

49 Ndipo 15 monga tabvaia fanizo la wanthakayo, tidzabvalanso fanizo la wakumwambayo.

50 Koma ndinena ici, abale, kuti 16 thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena cibvundi sicilowa cisabvundi.

51 Taonani, ndikuuzani cinsinsi; 17 sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,

52 m'kamphindi, m'kutwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti 18 lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osabvunda, ndipoife tidzasandulika.

53 Pakuti cobvunda ici ciyenera kubvala cisabvundi, ndi 19 caimfa ici kubvala cosafa.

54 Ndipo pamene cobvunda ici cikadzabvala cisabvundi ndi caimfa ici cikadzabvala cosafa, pamenepo padzacitika mau olembedwa, 20 Imfayo yamezedwa m'cigonjetso.

55 21 Imfawe, cigonjetso cako ciri kuti? Imfawe, mbola yako iri kuti?

56 Koma mbola ya imfa ndiyo ucimo; koma 22 mphamvu ya ucimo ndiyo cilamulo:

57 koma 23 ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife cigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.

58 Cifukwa cace, abale anga okondedwa, 24 khalani okhazikika, osasunthika, akucuruka mu ncbitoya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kucititsa kwanu sikuli cabe mwa Ambuye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16