1 Akorinto 16 BL92

Zopereka za kwa Akristu a ku Yerusalemu

1 Koma za copereka ca kwa oyera mtima, mongandinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero citani inunso.

2 Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha; monga momwe anapindula, kuti zopereka zisacitike pakudza ine.

3 Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.

4 Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.

Za maulendo akudza, ndi malankhulano a Paulo

5 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Makedoniya; pakuti ndidzapyola Makedoniya;

6 ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yacisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kuli konse ndipitako,

7 Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.

8 Koma ndidzakhaia ku Efeso kufikira Penteskoste,

9 Pakuti panditsegukira pa khomo lalikuru ndi locititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.

10 Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira nchito ya Ambuye, monganso ine;

11 cifukwa cace munthu asampeputse, Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze: kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale,

12 Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sicinali cifuniro cace kuti adze tsopano, koma adzafika pameneaona nthawi.

13 Dikirani, cirimikani m'cikhulupiriro; dzikhalitseni amuna, limbikani.

14 Zanu zonse zicitike m'cikondi.

15 Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefana, kuti ali cipatsocoundukula ca Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),

16 kuti inunso mubvomere otere, ndi yense wakucita nao, ndi kugwiritsa nchito.

17 Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefana, ndi Fortunato, ndi Akayiko; cifukwa iwo anandikwaniritsa cotsalira canu.

18 Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; cifukwa cace muzindikire otere.

19 Mipingo ya ku Asiya ilankhula inu. Akulankhulani ndithu inu mwa Ambuye, Akula ndi Priska, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao,

20 Akulankhulani inu abale onse. Lankhulanani ndi kupsompsona kopatulika.

21 Kulankhula kwa ine Paulo ndi dzanja langa.

22 Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.

23 Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu cikhale ndi inu.

24 Cikondi canga cikhale ndi inu nonse mwa Kristu Yesu. Amen.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16