Aroma 16 BL92

Zolawirana

1 Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya;

2 kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zili zonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.

3 Mulankhule Priska ndi Akula, anchito anzanga m'Kristu Yesu,

4 amene anapereka khosi lao cifukwa ca moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu;

5 ndipo mulankhule Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Mulankhule Epeneto wokondedwa wanga, ndiye cipatso coundukula ca Asiya ca kwa Kristu,

6 Mulankhule Mariya amene anadzilemetsa ndi nchito zambiri zothandiza inu.

7 Mulankhule Androniko ndi Yuniya, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali omveka mwa amitumwi, amenenso ananditsogolera ine mwa Kristu.

8 Mulankhule Ampliato wokondedwa wanga mwa Ambuye.

9 Mulankhule Urbano wanchito mnzathu mwa Kristu, ndi Staku wokondedwa wanga,

10 Mulankhule Apele, wobvomerezedwayo mwa Kristu, Mulankhule iwo a kwa Aristobulo.

11 Mulankhule Herodiona, mbale wanga. Mulankhule iwo a kwa Narkiso, amene ali mwa Ambuye.

12 Mulankhule Trufena, ndi Trufosa amene agwiritsa nchito mwa Ambuyeo Mulankhule. Persida, wokondedwayo amene anagwiritsa nchito zambiri mwa Ambuye.

13 Mulankhule Rufo, wosankhidwayo mwa Ambuye, ndi amai wace ndi wanga.

14 Mulankhule Asunkrito, Felego, Herme, Patroba, Henna ndi abale amene ali nao.

15 Mulankhule Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mlongo wace, ndi Olumpa, ndi oyeramtima onse ali pamodzi nao.

16 Mulankhulane wina ndi mnzace ndi kupsompsona kopatulika. Mipingo yonse ya Kristu ikulankhulani inu.

17 Ndipo ndikudandaulirani; abale, yang'anirani iwo akucita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi ciphunzitsoco munaciphunzira inu; ndipopotolokani pa iwo.

18 Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Kristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asoceretsamitiina ya osalakwa.

19 Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Cifukwa cace ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.

20 Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.

21 Timoteo wanchito mnzanga akulankhulani inu; ndi Lukiyo ndi Yasoni ndi Sosipatro, abale anga.

22 Ine Tertio, ndirikulemba kalata ameneyu, ndikulankhulani inu mwa Ambuye.

23 Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Eklesia yense wa Ambuye, akulankhulani inu. Erasto, ndiye woyang'anira mudzi, akulankhulani inu, ndiponso Kwarto mbaleyo.

25 Ndipo kwa iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa uthenga wanga wabwino, ndi kulalildra kwa Yesu Kristu, monga mwa bvumbulutso la cinsinsi cimene cinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,

26 komai caonetsedwa tsopano, ndi kudziwidwa kwa anthu a mitundu yonse mwa malembo a aneneriwo, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti amvere cikhulupiriro;

27 kwa Mulungu wanzeru Yekha Yekha, mwa Yesu Kristu, kwa Yemweyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16