Aroma 8 BL92

Mayo watha watsopano mwa Kristu

1 Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.

2 Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.

3 Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m'thupi;

4 kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.

5 Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:

6 pakuti cisamaliro ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.

7 Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero.

8 Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.

9 Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu.

10 Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.

11 Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.

Ife ndife ana a Mulungu

12 Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi;

13 pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za thupi, mudzakhala ndi moyo.

14 Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu,

15 Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,

16 Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;

17 ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.

Zolengedwa zonse zilindira ana a Mulungu

18 Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

19 Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilimilia bvumbulutso la ana a Molungu.

20 Pakuti colengedwaco cagonietsedwa kuutsiru, cosafuna mwini, koma cifukwa ca iye amene anacigonjetsa,

21 ndi ciyembekezo kuti colengedwa comwe cidzamasulidwa ku ukapolo wa cibvundi, ndi kolowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu,

22 Pakuti tidziwa kuti colengedwa conse cibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.

23 Ndipo si cotero cokha, koma ife tomwe, tiri nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo ciomboledwe ca thupi lathu.

24 Pakuti ife tinapolumutsidwa ndi ciyembekezo; koma ciyembekezo cimene cioneka si ciri ciyembekezo ai; pa kuti ayembekezera ndani cimene acipenya?

25 Koma ngati tiyembekezera cimene: siticipenya, pomwepo ticilindirira ndi cipiriro.

26 Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti cimene tizipempha monga ciyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwiniatipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;

27 ndipo iye amene asanthula m'mitima adziwa cimene acisamalira Mzimu, cifukwa apempherera oyera mtima monga mwa cifuno ca Mulungu.

28 Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace.

29 Cifukwa kuti iwo 1 amene iye anawadziwiratu, 2 iwowa anawalamuliratu 3 afanizidwe ndi cifaniziro ca Mwana wace, kuti 4 iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;

30 ndipo amene iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene iye anawayesa olungama, 5 iwowa anawapatsanso olemerero.

Mulungu ali nafe, adzatitsutsa ndani

31 Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? 6 Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

32 iye amene sanatimana Mwana wace wa iye yekha, koma 7 anampereka cifukwa ca ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?

33 Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? 8 Mulungu ndiye ameneawayesa olungama;

34 9 ndani adzawatsutsa? Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, 10 amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, 11 amenenso atipempherera ife.

35 Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi?

36 Monganso kwalembedwa,12 Cifukwa ca Inu tirikuphedwa dzuwa lonse;Tinayesedwa monga nkhosa zakupha,

37 Koma 13 m'zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda.

38 Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu,

39 ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16