Aroma 10 BL92

Ayuda anataya cilungamo ca Mulungu

1 Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.

2 Pakuti ndiwacitira iwo umboni kuti a ali ndi cangu ca kwa Mulungu, koma si monga mwa cidziwitso.

3 Pakuti pakusadziwa cilungamo ca Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa cilungamo ca iwo okha, iwo sanagonja ku cilungamo ca Mulungu.

4 Pakuti Kristu ali cimariziroca lamulo kulinga kucilungamo kwa amene ali yense akhulupira,

5 Pakuti Mose walemba kuti munthu amene acita cilungamo ca m'lamulo, adzakhala naco ndi moyo.

6 Koma cilungamo ca cikhulupiriro citero, Usamanena mumtima mwako, Adzakwera ndani Kumwambako? ndiko, kutsitsako Kristu;

7 kapena, Adzatsikira ndani kudzenieko? ndiko, kukweza Kristu kwa akufa.

8 Koma citani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a cikhulupiriro, amene ife tiwalalikira:

9 kuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:

10 pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo cilungamo; ndi m'kamwa abvomereza kutengapo cipulumutso

11 Pakuti lembo litere, Amene ali yense akhulupirira iye, sadzacita manyazi.

12 Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawacitira zolemera onse amene aitana pa iye;

13 pakuti, amene ali yense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

14 Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?

15 ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.

16 Koma sanamvera Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife?

17 Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu.

18 Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu,Liu lao linaturukira ku dziko lonse lapansi,Ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.

19 Koma nditi, Kodi Israyeli alibe kudziwa? Poyamba Mose anena,Ine ndidzacititsa inu nsanje ndi iwo amene sakhala mtundu wa anthu,Ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira.

20 Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati,Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifuna;Ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunsa.

21 Koma kwa Israyeli anena, Dzuwa lonse ndinatambalitsira manja anga kwa anthu osamvera ndi okanakana.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16