Aroma 1 BL92

1 PAULO, kapolowa Yesu Kristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,

2 umene iye analonjeza kale ndi mau a ananeri ace m'malembo oyera,

3 wakunena za Mwana wace, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,

4 amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa ciyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Kristu Ambuye wathu;

5 amene ife tinalandira naye cisomo ndi utumwi, kuti amvere cikhulupiriro anthu a mitundu yonse cifukwa ca dzina lace;

6 mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Kristu;

7 kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Cisomo cikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.

Paulo ayamika Mulungu cifukwa ca cikhulupiriro ca Aroma. Afuna kuceza nao

8 Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Kristu cifukwa ca inu nonse, cifukwa kuti mbiri ya cikhulupiriro canu idamveka pa dziko lonse lapansi.

9 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, m'Uthenga Wabwino wa Mwana wace, kuti kosalekeza ndikumbukila inu, ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga,

10 ngati nkutheka tsopano mwa cifuniro ca Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu.

11 Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;

12 ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa cikhulupiriro ca ife tonse awiri, canu ndi canga.

13 Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawiri kawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.

Uthenga wace wa Paulo wakuti anthu ayesedwa olungama mwa cikhalupiriro

14 Ine ndiri wamangawa wa Ahelene ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa.

15 Cotero, momwe ndingakhoze ine, ndirikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma.

16 Pakuti Uthenga Wabwino sundicititsa manyazi; pakuti uti mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene.

17 Pakuti m'menemo caonetsedwa cilungamoca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro.

Kuipitsitsa kwa anthu

18 Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wocokera Kumwamba, uonekera pa cisapembedzo conse ndi cosalungama ca anthu, amene akanikiza pansi coonadi m'cosalungama cao;

19 cifukwa codziwika ca Mulungu caonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anacionetsera kwa iwo.

20 Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;

21 cifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamcitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pace m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira,

22 Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;

23 nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi cifaniziro ca munthu woonongeka ndi ca mbalame, ndi ca nyama zoyendayenda, ndi ca zokwawa.

24 Cifukwa cace Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kucititsana matupi ao wina ndi mnzace zamanyazi;

25 amenewo anasandutsa coonadi ca Mulungu cabodza napembedza, natumikira colengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.

26 Cifukwa ca ici Mulungu anawapereka iwo 1 ku zilakolako za manyazi; pakuti angakhale akazi ao anasandutsa macitidwe ao a cibadwidwe akhale macitidwe osalingana ndi cibadwidwe:

27 ndipo cimodzimodzinso amuna anasiya macitidwe a cibadwidwe ca akazi, natenthetsana ndi colakalaka cao wina ndi mnzace, amuna okhaokha anacitirana camanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.

28 Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'cidziwitso cao, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukacita zinthu zosayenera;

29 anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, cinyengo, udani;

30 akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, acipongwe, odzitama, amatukutuku, ovamba zoipa, osamvera akuru ao,

31 opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda cikondi ca cibadwidwe, opanda cifundo;

32 amene ngakhale adziwa kuweruza kwace kwa Mulungu, kuti iwo 2 amene acita zotere ayenera imfa, azicita iwo okha, ndiponso abvomerezana ndi iwo akuzicita.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16