1 Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofoka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.
2 Yense wa ife akondweretse mnzace, kumcitira zabwino, zakumlimbikitsa.
3 Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakuoyoza iwe Inagwa pa Ine,
4 Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa cipiriro ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo.
5 Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu;
6 kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.
7 Cifukwa cace mulandirane wina ndi mnzace, monganso Kristu anakulandirani inu, kukacitira Mulungu ulemerero.
8 Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, cifukwa ca coonadi ca Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,
9 ndi kuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, cifukwa ca cifundo; monga kwalembedwa,Cifukwa ca icindidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu,Ndidzayimbira dzina lanu.
10 Ndiponso anena,Kondwani, amitundu inu, pamodzindi anthu ace.
11 Ndiponso,Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse;Ndipo anthu onse amtamande.
12 Ndiponso, Yesaya ati,Padzali muzu wa Jese,Ndi iye amene aukira kucita ufumu pa anthu amitundu;Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.
13 Ndipo Mulungu wa ciyembekezo adzaze inu ndi cimwemwe conse ndi mtendere m'kukhulupira, kuti mukacuruke ndi ciyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
14 Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzace.
15 Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, cifukwa ca cisomo capatsidwa kwa ine ndi Mulungu,
16 kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Kristu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwace kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.
17 Cifukwa cace ndiri naco codzitamandira ca m'Kristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu.
18 Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Kristu sanazicita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi nchito,
19 mu mphamvu ya zizindikilo ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Kristu;
20 ndipo cotero ndinaciyesa cinthu caulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo Kristu asanachulldwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.
21 Koma monga kwalembedwa,Iwo amene uthenga wace sunawafikire, adzaona,Ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa.
22 Cifukwa cacenso ndinaletsedwa kawiri kawiri kudza kwa inu;
23 koma tsopano, pamene ndiribe malo m'maiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero,
24 pamene pali ponse ndidzapita ku Spanya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.
25 Koma 1 tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndirikutumikira oyera mtima.
26 Pakuti 2 kunakondweretsa a ku Makedoniya ndi Akaya kucereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.
27 Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. 3 Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikica iwo ndi zinthu zathupi.
28 Koma pamene ndikatsiriza ici, ndi kuwasindikizira iwo cipatso ici, ndidzapyola kwanu kupita ku Spanya.
29 Ndipo 4 ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m'kudzaza kwace kwa cidalitso ca Kristu.
30 Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mzimu, kuti 5 mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu cifukwa ca ine;
31 kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;
32 6 kuti ndi cimwemwe ndikadze kwa inu mwa cifuno ca Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.
33 Ndipo 7 Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.