Aroma 11 BL92

Mulungu sanataya Aisrayeli onse

1 Cifukwa cace ndinena, Mulungu anataya anthu ace kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndiri M-israyeli, wa mbeu ya Abrahamu, wa pfuko la Benjamini.

2 Mulungu sanataya anthu ace amene iye anawadziwiratu, Kapena simudziwa kodi cimene lembo linena za Eliya? kuti anaumirira Mulungu poneneza Israyeli, kuti,

3 Ambuye, anawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.

4 Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu amunazikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadira Baala.

5 Coteronso nthawi yatsopano ciripo cotsalira monga mwa kusankha kwa cisomo.

6 Koma ngati kuli ndi cisomo, sikulinso ndinchito ai; ndipo pakapanda kutero, cisomo sicikhalanso cisomo.

7 Ndipo ciani tsono? ici cimene Israyeli afunafuna sanacipeza; koma osankhidwawo anacipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;

8 monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.

9 Ndipo Davide akuti,Gome lao likhale kwa iwo, ngati msampha, ndi ngati diwa,Ndi monga cokhumudwitsa, ndi cowabwezera cilango;

10 Maso ao adetsedwe, kuti asapenye,Ndipo muweramitse msana wao masiku onse.

11 Cifukwa cace ndinena, Anakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ai; koma ndi kulakwa kwao cipulumutso cinadza kwa anthu akunja, kudzacititsa iwo nsanje.

12 Ndipo ngati kulakwa kwao kwatengera dzikolapansi zolemera, ndipo kucepa kwao klltengera anthu amitundu zolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao?

Potsiriza Mulungu adzapulumutsa Israyeli

13 Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndiri mtumwi wa anthu amitundu, millemekeza utumiki wanga;

14 kuti ngati nkutheka ndikacititse nsanje amenewo a mtundu wanga; ndi kupulumutsa ena a iwo.

15 Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuvanianitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakucokera kwa: akufa?

16 Ndipo ngati zoundukula ziri zopatulika, coteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, coteronso nthambi.

17 Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wazitona wa kuthengo, unamezetsanidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ace a mtengowo,

18 usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu.

19 Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikamezetsanidwe nao.

20 Cabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi cikhulupiriro cako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:

21 pakuti ngati Mulungu sanaleka nthambi za mtundu wace, inde sadzakuleka iwe.

22 Cifukwa cace onani cifatso ndi kuuma mtima kwace kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwace; koma kwa iwe cifatso cace ca Mulungu, ngati ukhala cikhalire m'eifatsomo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.

23 Ndipo iwonso, ngati sakhala cikhalire ndi cisakhulupiriro, adzawamezanitsanso.

24 Pakuti ngati iwe unasadzidwa ku mtengo wazitona wa mtundu wa kuthengo, ndipo unamezetsanidwa ndi mtengo wazitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wace, adzamezetsanidwa ndi mtengo wao womwewo wazitona?

25 Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa cinsinsi ici, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israyeli, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;

26 ndipo cotero Israyeli yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti,Adzaturuka ku Ziyoni Mpulumutsi;Iye adzacotsa zamwano kwa Yakobo:

27 Ndipo ici ndi cipangano canga ndi iwo,Pamene ndidzacotsa macimo ao.

28 Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, cifukwa ca inu; koma kunena za cisankhidwe, z ali okondedwa, cifukwa ca makolo.

29 Pakuti 1 mphatso zace ndi kuitana kwace kwa Mulungu sizilapika.

30 Pakuti 2 monga inunso kale simunamvera Mulungu, koma tsopano mwalandira cifundo mwa kusamvera kwao,

31 coteronso iwo sanamvera tsopano, kuti iwonso akalandire cifundo, cifukwa ca cifundo ca kwa inu.

32 Pakuti 3 Mulungu anatsekera pamodzi onse m'kusamvera, kuti akacitire onse cifundo.

Ulemu waukuru wa Mulungu

33 Ha! kuya kwace kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwace kwa Mulungu! 4 Osasanthulikadi maweruzo ace, ndi njira zace nzosalondoleka!

34 Pakuti 5 anadziwitsa ndani mtima wace wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wace ndani?

35 Ndipo 6 anayamba ndani kumpatsa iye, ndipo adzambwezeranso?

36 Cifukwa 7 zinthu zonse zicokera kwa iye, zicitika mwa iye, ndi kufikira kwa iye. 8 K wa Iyeyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16