Aroma 3 BL92

Kuposa kwace kwa Myuda Mulungu ali wolungama

1 Ndipo potero Myuda aposa Dinji? Kapena mdulidwe upindulanji?

2 Zambiri monse monse: coyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo.

3 Nanga bwanji ngati ena sanakhulupira? Kodi kusakhulupira kwao kuyesa cabe cikhulupiriko ca Mulungu?

4 Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa,Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu,Ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa.

5 Koma ngati cosalungama cathu citsimikiza cilungamo ca Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (ndilankhula umo anenera munthu).

6 Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi?

7 Pakuti ngati coonadi ca Mulungu cicurukitsa ulemerero wacecifukwa ca bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wocimwa?

8 Ndipo tilekerenji kunena, Ticite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.

Anthu onse agwidwa ndi zoipa

9 Ndipo ciani tsono? kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Ahelene omwe, kuti onsewa agwidwa ndi ucimo;

10 monga kwalembedwa,Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi;

11 Palibe mmodzi wakudziwitsa, Palibe mmodzi wakuloodola Mulungu;

12 Onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pace;Palibe mmodzi wakucita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.

13 M'mero mwao muli manda apululu;Ndi lilime lao amanyenga; Ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;

14 M'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;

15 Miyendo yao icita liwiro kukhetsa mwazi;

16 Kusakaza ndi kusauka kuli m'njira zao;

17 Ndipo njira ya mtendere sanaidziwa;

18 Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.

19 Ndipo tidziwa kuti zinthu ziri zonse cizinena cilamulo cizilankhulira iwo ali naco cilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;

20 cifukwa kuti pamaso pace palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi Debito za lamulo; pakuti ucimo udziwika ndi lamulo.

Tilungamitsidwa mwa kukhulupirira Yesu Kristu

21 Koma tsopano cilungamo ca Mulungu caoneka copanda lamulo, cilamulo ndi aneneri acitira ici umboni;

22 ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana;

23 pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

24 ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu;

25 amene Mulungu anamuika poyera akhale cotetezera mwa cikhulupiriro ca m'mwazi wace, kuti aonetse cilungamo cace, popeza Mulungu m'kulekerera kwace analekerera macimo ocitidwa kale lomwe;

26 kuti aonetse cilungamo cace m'nyengo yatsopano; kuti iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu,

27 Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La nchito kodi? lai; koma ndi lamulo la cikhulupiriro.

28 Pakuti timuyesa munthu wohmgama cifukwa ca cikhulupiriro, wopanda nchito za lamulo.

29 Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okha okha kodi? si wao wa amitundunso kodi? Bya, wa amitundunso:

30 ngatitu ndiye Mulungu mmodzi, amene adzawayesa amdulidwe olungama ndi cikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa cikhulupiriro,

31 Potero kodi lamulo tiyesa cabe mwa cikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16